Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 28:23-29 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

23. Cherani inu makutu, imvani mau anga; mverani, imvani kulankhula kwanga.

24. Kodi mlimi amalimabe kuti abzale? kodi amacocolabe, ndi kuswa zibuma za nthaka?

25. Atakonza tyatyatya pamwamba pace, kodi safesa ponse mawere, ndi kumwazamwaza citowe, nafesa tirigu m'mizere ndi barele m'malo ace osankhika, ndi mcewere m'maliremo?

26. Pakuti Mulungu wace amlangiza bwino namphunzitsa.

27. Pakuti sapuntha mawere ndi copunthira cakuthwa, ngakhale kuzunguniza njinga ya gareta pacitowe; koma amakulunga mawere ndi munsi, naomba citowe ndi cibonga.

28. Tirigu wa mkate aperedwa; pakuti samampuntha osaleka; ngakhale kuyendetsapo njinga ya gareta wace, ngakhale kumphwanya ndi ziboda za akavalo ace sapera.

29. Icinso cifumira kwa Yehova wa makamu, uphungu wace uzizwitsa ndi nzeru yace impambana.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 28