Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 28:1-5 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Tsoka kwa korona wakunyada wa oledzera a Efraimu, ndi kwa duwa lakufota la ulemerero wace wokongola, limene liri pamutu paiwo, amene agwidwa ndi vinyo, m'cigwa ca nthaka yabwino.

2. Taonani, Ambuye ali ndi wina wamphamvu wolimba; ngati cimphepo ca matalala, mkuntho wakuononga, ngati namondwe wa madzi amphamvu osefukira, adzagwetsa pansi ndi dzanja lamphamvu.

3. Korona wakunyada wa oledzera a Efraimu adzaponderezedwa;

4. ndi duwa lakufota la ulemerero wace wokongola, limene liri pamutu pa cigwa ca nthaka yabwino, lidzakhala ngati nkhuyu yoyamba kuca malimwe asanafike; polona wakupenya imeneyo, amaidya iri m'dzanja lace.

5. Tsiku limenelo Yehova wa makamu adzakhala korona wa ulemerero, ndi korona wokongola kwa anthu ace otsala:

Werengani mutu wathunthu Yesaya 28