Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 27:1-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Tsiku limenelo Yehova ndi lupanga lace lolimba ndi lalikuru ndi lamphamvu adzalanga nangumi njoka yotamanga, ndi nangumi njoka yopindika-pindika; nadzapha cing'ona cimene ciri m'nyanja.

2. Tsiku limenelo: munda wa mphesa wavinyo, yimbani inu za uwo.

3. Ine Yehova ndiusunga uwo; ndidzauthirira madzi nthawi zonse; ndidzausunga usiku ndi usana, kuti angauipse.

4. Ndiribe ukali; ndani adzalimbanitsa lunguzi ndi minga ndi Ine kunkhondo? ndiziponde ndizitenthe pamodzi.

5. Kapena mlekeni, agwire mphamvu zanga, nacite nane mtendere; inde, acite nane mtendere.

6. M'mibadwo ikudzayo Yakobo adzamera mizu; Israyeli adzaphuka ndi kucita mphundu; ndipo iwo adzadzaza ndi zipatso pa dziko lonse lapansi.

7. Kodi Mulungu wakantha Yakobo, monga umo anawakanthira akumkanthawo? kapena kodi iye waphedwa malinga ndi kuphedwa kwa iwo amene anaphedwa ndi iye?

Werengani mutu wathunthu Yesaya 27