Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 24:19-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

19. Dziko lapansi lasweka ndithu, dziko lapansi lasungunukadi, dziko lapansi liri kugwedezeka kopambana.

20. Dziko lapansi lidzacita dzandi dzandi, ngati munthu woledzera, ndi kunjenjemera, ngati cilindo; ndi kulakwa kwace kudzalilemera, ndipo lidzagwa losaukanso.

21. Ndipo padzali tsiku limenelo, kuti Yehova adzazonda kumwamba khamu la kumwamba, ndi mafumu a dziko lapansi.

22. Ndipo iwo adzasonkhanitsidwa pamodzi, monga ndende zimasonkhanitsidwa m'dzenje, ndi kutsekeredwa m'kaidi, ndipo atapita masiku ambiri adzawazonda.

23. Pompo mwezi udzanyazitsidwa, ndi dzuwa lidzakhala ndi manyazi, pakuti Yehova wa makamu adzalamulira caulemerero m'phiri la Ziyoni, ndi m'Yerusalemu, ndi pamaso pa akuru akuru ace.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 24