Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 21:9-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. ndipo taonani, kuno kulinkudza khamu la amuna, apaakavalo awiri awiri. Ndipo iye anayankha nati, Babulo wagwa, wagwa; ndi mafano onse osema a milungu yace asweka, nagwa pansi.

10. Kuomba kwanga nanga, ndi za pa dwale langa: cimene ine ndinacimva kwa Yehova wa makamu Mulungu wa Israyeli, ndanena kwa inu.

11. Katundu wa Duma.Wina aitana kwa ine kucokera ku Seiri, Mlonda, nthawi yanji ya usiku? Mlonda, nthawi yanji ya usiku?

12. Mlonda anati, Kuli kuca, koma kukali usiku; mukafuna kufunsa, funsani, bwerani, idzani.

13. Katundu wa pa Arabiya.M'nkhalango ya m'Arabiya mudzagona, inu makamu oyendayenda a Dedani.

14. Mucingamire akumva ludzu ndi madzi; okhala m'dziko la Tema ananka kukomana ndi othawa ndi cakudya cao.

15. Pakuti iwo anathawa malupanga, malupanga osololedwa, ndi mauta-olifuka ndi nkhondo yobvuta.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 21