Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 19:9-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Komanso iwo amene agwira nchito yakupala bwazi, ndi iwo amene aomba nsaru yoyera, adzakhala ndi manyazi.

10. Ndipo maziko ace adzasweka, onse amene agwira nchito yolipidwa adzabvutidwa mtima.

11. Akalonga a Zoani apusa ndithu; uphungu wa aphungu anzeru a Farao wasanduka wopulukira; bwanji iwe unena kwa Farao, Ine ndine mwana wa anzeru, mwana wa mafumu akale?

12. Nanga tsopano anzeru ali kuti? akuuze iwe tsopano; adziwe cimene Yehova wa makamu watsimikiza mtima kucitira Aigupto.

13. Akalonga a Zoani apusa, akalonga a Nofi anyengedwa; iwo asoceretsa Aigupto, amene ali mwala wa pangondya wa mapfuko ace.

14. Yehova wasanganiza mzimu wa kusaweruzika pakati pace; ndipo iwo asoceretsa Aigupto m'nchito zonse zace, monga mwamuna woledzera ayenda punzipunzi posanza pace.

15. Aigupto sadzakhala ndi nchito, imene mutu pena mcira, pena nthambi ya kanjedza, pena mlulu zidzaigwira.

16. Tsiku limenelo Aigupto adzanga akazi; ndipo adzanthunthumira ndi kuopa, cifukwa ca kugwedeza kwa dzanja la Yehova wa makamu, limene Iye agwedeza pamwamba pace.

17. Ndipo dziko la Yuda lidzaopsa Aigupto, yense wakulichula adzamtembenukira mwamantha, cifukwa ca uphungu wa Yehova wa makamu, aupanga pa dzikolo.

18. Tsiku limenelo padzakhala midzi isanu m'dziko la Aigupto yolankhula cinenero ca Kanani, ndi yolumbira, Pali Yehova wa makamu; wina udzachedwa, Mudzi wa cionongeko.

19. Tsiku limenelo padzakhala guwa la nsembe la Yehova pakati pa dziko la Aigupto, ndi coimiritsa ca Yehova m'malire ace.

20. Ndipo cidzakhala cizindikiro ndi mboni ya Yehova wa makamu m'dziko la Aigupto; pakuti iwo adzalirira kwa Yehova, cifukwa ca osautsa, ndipo Iye adzawatumizira mpulumutsi, ndi wamphamvu, nadzawapulumutsa.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 19