1. Katundu wa Aigupto.Taonani, Yehova wakwera pamwamba pa mtambo wothamanga, nadza ku Aigupto; ndi mafano a Aigupto adzagwedezeka pakufika kwace, ndi mtima wa Aigupto udzasungunuka pakati pace.
2. Ndipo ndidzapikisanitsa Aaigupto; ndipo adzamenyana wina ndi mbale wace, ndi wina ndi mnansi wace; mudzi kumenyana ndi mudzi, ndi ufumu kumenyana ndi ufumu.
3. Ndipo mzimu wa Aigupto adzakhala wacabe pakati pace; ndipo Ine ndidzaononga uphungu wace; ndimo iwo adzafunafuna mafano ndi anyanga, ndi alauli, ndi obwebweta.
4. Ndipo ndidzapereka Aigupto m'manja mwa mbuye wankharwe; ndi mfumu yaukali idzawalamulira, ati Ambuye, Yehova wa makamu.
5. Ndipo madzi adzaphwa m'nyanja yaikuru, ndipo nyanja yoyendamo madzi idzaphwa, niuma.
6. Ndipo nyanja zidzanunkha; mitsinje ya Aigupto idzacepa, niuma; bango ndi mlulu zidzafota.