Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 19:1-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Katundu wa Aigupto.Taonani, Yehova wakwera pamwamba pa mtambo wothamanga, nadza ku Aigupto; ndi mafano a Aigupto adzagwedezeka pakufika kwace, ndi mtima wa Aigupto udzasungunuka pakati pace.

2. Ndipo ndidzapikisanitsa Aaigupto; ndipo adzamenyana wina ndi mbale wace, ndi wina ndi mnansi wace; mudzi kumenyana ndi mudzi, ndi ufumu kumenyana ndi ufumu.

3. Ndipo mzimu wa Aigupto adzakhala wacabe pakati pace; ndipo Ine ndidzaononga uphungu wace; ndimo iwo adzafunafuna mafano ndi anyanga, ndi alauli, ndi obwebweta.

4. Ndipo ndidzapereka Aigupto m'manja mwa mbuye wankharwe; ndi mfumu yaukali idzawalamulira, ati Ambuye, Yehova wa makamu.

5. Ndipo madzi adzaphwa m'nyanja yaikuru, ndipo nyanja yoyendamo madzi idzaphwa, niuma.

6. Ndipo nyanja zidzanunkha; mitsinje ya Aigupto idzacepa, niuma; bango ndi mlulu zidzafota.

7. Madambo ovandikana ndi Nile, pafupi ndi gombe la Nile, ndi zonse zobzyala pa Nile zidzauma, nizicotsedwa, zosakhalanso konse.

8. Asodzinso adzalira, ndi onse oponya mbedza m'Nile adzaliralira, ndi onse oponya makoka m'madzi, adzalefuka.

9. Komanso iwo amene agwira nchito yakupala bwazi, ndi iwo amene aomba nsaru yoyera, adzakhala ndi manyazi.

10. Ndipo maziko ace adzasweka, onse amene agwira nchito yolipidwa adzabvutidwa mtima.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 19