Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 17:6-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Koma mudzasiyidwa m'menemo khunkha, monga ngati kugwedeza kwace kwa mtengo waazitona, zipatso ziwiri pena zitatu m'nsonga ya nthambi yosomphoka, zinai pena zisanu m'nthambi za kunthemba, za mtengo wobalitsa, ati Yehova, Mulungu wa Israyeli.

7. Tsiku limenelo munthu adzayang'ana kwa Mlengi wace, ndipo maso ace adzalemekeza Woyera wa Israyeli.

8. Ndipo iye sadzayang'ana pa maguwa a nsembe, nchito ya manja ace, ngakhale kulemekeza cimene anacipanga ndi zala zace, ngakhale zifanizo pena mafano a dzuwa.

9. Tsiku limenelo midzi yace yolimba idzakhala ngati mabwinja a m'nkhalango, ndi a pansonga pa phiri, osiyidwa pamaso pa ana a Israyeli; ndipo padzakhala bwinja.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 17