Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 17:10-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Cifukwa iwe waiwala Mulungu wa cipulumutso cako, sunakumbukira thanthwe la mphamvu zako; cifukwa cace iwe waoka mitengo yokondweretsa, waokapo zipinjiri zacilendo;

11. tsiku lako looka uzingapo mpanda, nuphukitsa mbeu zako m'mawa mwace; mulu wa masika udzaoneka tsiku lakulira ndi la cisoni cothetsa nzeru.

12. Ha, phokoso la mitundu yambiri ya anthu ambiri, amene apfuula ngati kukukuma kwa nyanja: ndi kuthamanga kwa amitundu, akuthamanga ngati kuthamangakwa madzi amphamvu!

13. Mitundu ya anthu idzathamanga ngati kuthamanga kwa madzi ambirimbiri; koma Iye adzawadzudzula, ndipo iwo adzathawira patari, nadzapitikitsidwa monga mankhusu a pamapiri patsogolo pa mphepo, ndi monga pfumbi lokwetera patsogolo pa mkunthu wa mphepo.

14. Pa nthawi ya madzulo, taonani kuopsya; kusanace, iwo palibe. Ili ndi gawo la iwo amene atifunkha ndi ici ciwagwera omwe alanda zathu.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 17