Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 17:1-5 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Katundu wa Damasiko. Taonani, Damasiko wacotsedwa usakhalenso mudzi, ndimo udzangokhala muunda wopasudwa.

2. Midzi ya Aroeri yasiyidwa; idzakhala ya zoweta zogona pansi, opanda woziopsya.

3. Ku Efraimu sikudzakhalanso linga, ngakhale ufumu ku Damasiko, ngakhale otsala kwa Aramu; iwo adzakhala ngati ulemerero wa ana a Israyeli, ati Yehova wamakamu.

4. Ndipo padzakhala tsiku limenelo, kuti ulemerero wa Yakobo udzakhala wopyapyala, ndi kunenepa kwa thupi lace kudzaonda.

5. Ndipo padzakhala ngati wamasika alikumweta tirigu wosaceka, ndi dzanja lace lirikudula ngala; inde padzakhala ngati pamene wina akunkha ngala m'cigwa ca Refaimu.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 17