Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 16:9-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Cifukwa cace ndidzalira ndi kulira kwa Yazeri, cifukwa ca mpesa wa Sibima, ndidzakukhathamiza ndi misozi yanga, iwe Hesiboni ndi Eleale; cifukwa kuti pa zipatso zako za malimwe, ndi pa masika ako, mpfuu wankhondo wagwera.

10. Ndipo cikondwero ndi msangalalo zacotsedwa m'munda wapatsa zipatso; ndi m'minda ya mipesa simudzakhala kuyimba, ngakhale phokoso losangalala; palibe woponda adzaponda vinyo m'moponderamo; ndaleketsa mpfuu wa masika amphesa.

11. Cifukwa cace m'mimba mwanga mulirira Moabu, ngati mngoli, ndi za m'mtima mwanga zilirira Kiriheresi.

12. Ndipo padzakhala kuti pamene Moabu adzadzionetsa yekha, ndi kudzitopetsa pamsanje, ndipo kufika ku malo ace oyera kudzapemphera, sadzapindulapo kanthu.

13. Awa ndi mau amene Yehova adanena za Moabu nthawi zapitazo.

14. Koma tsopano Yehova wanena, nati, Zisanapite zaka zitatu monga zaka za wolembedwa nchito, ulemerero wa Moabu udzakhala wonyozeka, ndi khamu lalikuru lace, ndi otsala adzakhala ang'ongong'ono ndi acabe.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 16