Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 14:22-32 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

22. Ndipo Ine ndidzawaukira, ati Yehova wa makamu, ndi kuononga ku Babulo dzina ndi otsala, ndi mwana wamwamuna, ndi cidzukulu cacimuna, ati Yehova.

23. Ndidzayesapo pokhala nungu, ndi madziwe a madzi; ndipo ndidzasesapo ndi tsace la cionongeko, ati Yehova wa makamu.

24. Yehova wa makamu walumbira, nati, Ndithu monga ndaganiza, cotero cidzacitidwa; ndipo monga ndapanga uphungu, cotero cidzakhala;

25. kuti Ine ndidzatyola Asuri m'dziko langa, ndi pamwamba pa mapiri anga ndidzawapondereza; pomwepo gori lace lidzacoka pa iwo, ndi katundu wace adzacoka paphuzi pao.

26. Umenewu ndi uphungu wopangira dziko lonse; ndipo ili ndi dzanja lotambasulidwa pa amitundu onse.

27. Pakuti Yehova wa makamu wapanga uphungu, ndani adzauleketsa? ndi dzanja lace latambasulidwa, ndani adzalibweza?

28. Caka cimene mfumu Ahazi anamwalira katundu amene analipo.

29. Usakondwere, lwe Filistia, wonsewe, potyoka ndodo inakumenya; pakuti m'muzu wa njoka mudzaturuka mphiri, ndimo cipatso cace cidzakhala njoka yamoto youluka.

30. Ndi oyamba kubadwa a osauka adzadya, aumphawi nadzagona pansi osatekeseka; ndipo ndidzapha muzu wako ndi njala, ndi otsala ako adzaphedwa.

31. Lira, cipata iwe; pfuula, mudzi iwe; wasungunuka, Filistia wonsewe, pakuti utsi ucokera kumpoto, ndipo palibe wosokera m'mizere yace.

32. Ndipo adzayankhanji amithenga a amitundu? Kuti Yehova wakhazikitsa Ziyoni, ndipo m'menemo anthu ace obvutidwa adzaona pobisalira.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 14