Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 13:1-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Katundu wa Babulo, imene anaiona Yesaya mwana wa Amozi.

2. Kwezani mbendera pa phiri loti se, kwezani mau kwa iwo, kodolani kuti alowe m'zipata za akuru.

3. Ine ndalamulira opatulidwa anga, inde, ndaitana amphamvu anga, acite mkwiyo wanga, okondwerera ndi ukuru wanga.

4. Mau a khamu m'mapiri, akunga amtundu waukuru wa anthu, mau a phokoso la maufumu a mitundu yosonkhanidwa! Yehova wa makamu asonkhanitsa khamu kunkhondo.

5. Acokera m'dziko lakutari, ku malekezero a thambo, ngakhale Yehova, ndi zida za mkwiyo wace, kuti aononge dziko lonse.

6. Kuwani inu; pakuti tsiku la Yehova liri pafupi; lidzafika monga cionongeko cocokera kwa Wamphamvuyonse.

7. Cifukwa cace manja onse adzafoka, ndi mitima yonse ya anthu idzasungunuka;

8. ndipo adzaopa; zowawa ndi masauko zidzawagwira; ndipo adzamva zowawa, ngati mkazi wakubala; adzazizwa wina ndi wina; nkhope zao zidzanga malawi a moto.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 13