Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 11:1-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo padzaturuka mphukira pa tsinde la Jese, ndi nthambi yoturuka m'mizu yace idzabala zipatso;

2. ndipo mzimu wa Yehova udzambalira iye mzimu wanzeru ndi wakuzindikira, mzimu wa uphungu ndi mphamvu, mzimu wakudziwa ndi wakuopa Yehova;

3. ndipo adzakondwera nako kumuopa Yehova, ndipo sadzaweruza monga apenya maso, sadzadzudzula mwamphekesera:

4. koma ndi cilungamo adzaweruza aumphawi, nadzadzudzulira ofatsa a m'dziko moongoka; ndipo adzamenya dziko lapansi ndi cibonga ca kukamwa kwace, nadzapha oipa ndi mpweya wa milomo yace.

5. Ndipo cilungamo cidzakhala mpango wa m'cuuno mwace, ndi cikhulupiriko cidzakhala mpango wa pa zimpsyo zace.

6. Mmbulu udzakhala pamodzi ndi mwana wa nkhosa, ndipo nyalugwe adzagona pansi ndi mwana wa mbuzi; ndipo mwana wa ng'ombe ndi mwana wa mkango ndi coweta conenepa pamodzi; ndipo mwana wamng'ono adzazitsogolera.

7. Ndipo ng'ombe yaikazi ndi cirombo zidzadya pamodzi; ndipo ana ao ang'ono adzagona pansi; ndipo mkango udzadya udzu ngati ng'ombe.

8. Ndipo mwana wakuyamwa adzasewera pa una wa mamba, ndi mwana woleka kuyamwa adzaika dzanja lace m'pfunkha la mphiri.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 11