Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 10:26-33 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

26. Ndipo Yehova wa makamu adzamuutsira cikoti, monga m'kuphedwa kwa Midyani pa thanthwe la Orebu; ndipo cibonga cace cidzakhala pamwamba pa nyanja, ndipo adzaisamula monga anacitira Aigupto,

27. Ndipo padzakhala tsiku lomwelo, kuti katundu wace adzacoka pa phewa lako, ndi gori lace pakhosi pako; ndipo gori lidzathedwa cifukwa ca kudzoza mafuta.

28. Wafika ku Aiati, wapitirira kunka ku Migroni; pa Mikimasi asunga akatundu ace;

29. wapita pampata; wagona pa Geba, Rama anthunthumira; Gibeya wa Sauli wathawa.

30. Pfuula ndi mau ako iwe mwana wamkazi wa Galimu! tamva, iwe Laisa! iwe Anatoti wosauka!

31. Madimena ali wothawathawa; okhala m'Gebimu asonkhanakutiathawe.

32. Lero lomwe adzaima pa Nobu; agwedezera dzanja lace pa phiri la mwana wamkazi wa Ziyoni, phiri la Yerusalemu.

33. Taonani, Ambuye Yehova wa makamu adzasadza nthambi moopsya; ndipo zazitari msinkhu zidzadulidwa, ndipo zazitari zidzagwetsedwa.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 10