Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 10:18-25 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

18. Ndipo adzanyeketsa ulemerero wa m'nkhalango yace, ndi wa m'munda wace wopatsa bwino, moyo ndi thupi; ndipo padzakhala monga ngati pokomoka wonyamula mbendera.

19. Ndipo mitengo yotsala ya m'nkhalango yace idzakhala yowerengeka, kuti mwana ailembera.

20. Ndipo padzakhala tsiku lomwelo, kuti otsala a Israyeli, ndi iwo amene anapulumuka a nyumba ya Yakobo, sadzatsamiranso iye amene anawamenya; koma adzatsamira Yehova Woyera wa Israyeli, ntheradi.

21. Otsala adzabwera, otsala a Yakobo, kwa Mulungu wamphamvu.

22. Popeza ngakhale anthu anu Israyeli akunga mcenga wa kunyanja, otsala ao okha okha adzabwera; cionongeko catsimikizidwa, cilungamo cace cisefukira.

23. Pakuti Ambuye Yehova wa makamu adzacita cionongeko cotsimikizidwa pakati pa dziko lonse lapansi.

24. Cifukwa cace atero Ambuye; Yehova wa makamu, Inu anthu anga okhala m'Ziyoni, musaope Asuri; ngakhale amenya inu ndi cibonga, kapena kukusamulira iwe ndodo yace, monga amacitira Aigupto.

25. Pakuti patsala kamphindi, ndipo ukali udzathedwa ndi mkwiyo wanga wakuwaononga.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 10