Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 10:1-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Tsoka kwa iwo amene alamulira malamulo osalungama, ndi kwa alembi olemba mphulupulu;

2. kuwapatulira osowa kuciweruziro, ndi kucotsera anthu anga aumphawi zoyenera zao, kuti alande za akazi amasiye, nafunkhire ana amasiye!

3. Ndipo mudzacita ciani tsiku lakudza woyang'anira, ndi cipasuko cocokera kutari? mudzathawira kwa yani kufuna kuthangatidwa? mudzasiya kuti ulemerero wanu?

4. Adzangoweramira pansi pa andende, ndipo adzagwa pansi pa ophedwa. Mwa izi zonse mkwiyo wace sunacoke, koma dzanja lace liri citambasulire.

5. Iwe Asuri cibonga ca mkwiyo wanga, ndodo m'dzanja lace muli ukali wanga!

6. Ine ndidzamtumiza kumenyana ndi mtundu wosalemekeza, ndi pa anthu a mkwiyo wanga ndidzamlangiza, kuti afunkhe, agwire zolanda, awapondereze pansi, monga dothi la pamakwalala.

7. Koma iye safuna cotero, ndipo mtima wace suganizira cotero, koma mtima wace ulikufuna kusakaza, ndi kuduladula amitundu osawerengeka.

8. Popeza ati, Akalonga anga kodi sali onse mafumu?

9. Kodi Kalino sali wonga ngati Karikemesi? kodi Hamati sali ngati Aripadi? kodi Samariya sali ngati Damasiko?

10. Popeza dzanja langa lapeza maufumu a mafano, mafano ao osema anapambana ndi iwo a ku Yerusalemu ndi ku Samariya;

11. monga ndacitira Samariya ndi mafano ace, momwemo kodi sindidzacitira Yerusalemu ndi mafano ace?

12. Cifukwa cace padzaoneka, kuti pamene Ambuye atatha nchito yace yonse pa phiri la Ziyoni ndi pa Yerusalemu, ndidzalanga zipatso za mtima wolimba wa mfumu ya Asuri, ndi ulemerero wa maso ace okwezedwa.

13. Popeza anati, Mwa mphamvu ya dzanja langa ndacita ici, ndi mwa nzeru yanga; pakuti ine ndiri wocenjera; ndacotsa malekezero a anthu, ndalanda cuma cao, ndagwetsa monga munthu wolimba mtima iwo okhala pa mipando yacifumu;

14. dzanja langa lapeza monga cisa, cuma ca mitundu ya anthu, ndipo monga munthu asonkhanitsa mazira osiyidwa, ine ndasonkhanitsa dziko lonse lapansi, ndipo panalibe cogwedeza phiko, kapena cotsegula pakamwa, kapena colira pyepye.

15. Kodi nkhwangwa idzadzikweza yokha, pa iye amene adula nayo? kodi cocekera cidzadzikweza cokha pa iye amene acigwedeza, ngati cibonga ingamgwedeze iye amene ainyamula, ngati ndodo inganyamule kanthu popeza iri mtengo.

16. Cifukwa cace Ambuye, Yehova wa makamu, adzarumiza kuonda mwa onenepa ace; ndipo pansi pa ulemerero wace padzayaka kutentha, konga ngati kutentha kwa moto.

17. Ndipo kuwala kwa Israyeli kudzakhala moto, ndi Woyera wace adzakhala lawi; ndipo lidzatentha ndi kuthetsa minga yace ndi lunguzi wace tsiku limodzi.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 10