Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 9:1-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ha, mutu wanga ukadakhala madzi, ndi maso anga kasupe wa misozi, kuti usana ndi usiku ndilirire ophedwa a mwana wamkazi wa anthu anga!

2. Ha, ndikadakhala ndi cigono ca anthu aulendo m'cipululu; kuti ndisiye anthu anga, ndiwacokere, pakuti onse ali acigololo msonkhano wa anthu aciwembu.

3. Ndipo apinda lilime lao ngati uta wao, liname; koma akula mphamvu m'dzikomo, koma si pacoonadi; pakuti alinkunkabe nacita zoipa, ndipo sandidziwa Ine, ati Yehova.

4. Mucenjere naye yense mnansi wace, musakhulupirire yense mbale wace; pakuti abale onse amanyenga, ndipo anansi onse adzayenda ndi maugogodi.

5. Ndipo yense adzanyenga mnansi wace, osanena coonadi; aphunzitsa lilime lao kunena zonama; nadzithodwetsa kucita zoipa.

6. Ukhala pakati pa manyengo m'manyengo; akana kundidziwa, ati Yehova.

7. Cifukwa cace atero Yehova wa makamu, Taonani, ndidzawasungunula, ndi kuwayesa, pakuti ndidzacitanji, cifukwa ca mwana wamkazi wa anthu anga?

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 9