Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 7:9-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Kodi mudzapha, ndi kuba, ndi kucita cigololo, ndi kulumbira zonama, ndi kupereka nsembe kwa Baala, ndi kutsata milungu yina imene simunaidziwa,

10. ndi kudza ndi kuima pamaso panga m'nyumba yino, imene ichedwa dzina langa, ndi kuti, Talanditsidwa; kuti mucite zonyansa izi?

11. Kodi nyumba yino, imene ichedwa dzina langa, ikhala phanga la okwatula pamaso panu? Taona, Ine ndaciona, ati Yehova.

12. Koma pitani tsopano ku malo anga amene anali m'Silo, m'mene ndinaikamo dzina langa poyamba paja, ndi kuona cimene ndinacitira cifukwa ca zoipa za anthu anga Israyeli.

13. Ndipo tsopano, cifukwa munacita nchito zonsezi, ati Yehova, ndipo ndinanena kwa inu, ndi kuuka mamawa ndi kunena, koma simunamva; ndipo ndinakuitanani inu, koma simunayankha;

14. cifukwa cace ndidzaicitira nyumba iyi, imene ichedwa dzina langa, imene mukhulupirirayi, ndipo ndidzacitira malo amene ndinakupatsani inu ndi makolo anu, monga ndinacitira Silo.

15. Ndipo ndidzakucotsani inu pamaso panga, monga ndinacotsa abale anu onse, mbeu zonse za Efraimu.

16. Cifukwa cace iwe usapempherere anthu awa, usawakwezere iwo mpfuu kapena pemphero, usandipembedze; pakuti Ine sindidzakumvera iwe.

17. Kodi suona iwe cimene acicita m'midzi ya Yuda ndi m'miseu ya Yerusalemu?

18. Ana atola nkhuni, atate akoleza moto, akazi akanyanga ufa, kuti aumbe mikate ya mfumu yaikazi ya kumwamba, athirire milungu yina nsembe yothira, kuti autse mkwiyo wanga.

19. Kodi autsa mkwiyo wanga? ati Yehova; kodi sadziutsira okha manyazi a nkhope zao?

20. Cifukwa cace, ati Ambuye Mulungu, Taonani, mkwiyo wanga ndi ukali wanga udzathiridwa pa malo ano, pa anthu, ndi pa nyama, ndi pa mitengo ya m'munda, ndi pa zipatso zapansi; ndipo udzatentha osazima.

21. Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli; Ikani zopereka zopsereza zanu pa nsembe zophera zanu, nimudye nyama.

22. Pakuti sindinanena kwa makolo anu, tsiku lija ndinawaturutsa m'dziko la Aigupto, ngakhale kuwauza nsembe zopsereza kapena zophera;

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 7