Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 7:2-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. Ima m'cipata ca nyumba ya Yehova, lalikira m'menemo mau awa, ndi kuti, Tamvani mau a Yehova, inu nonse a Yuda, amene alowa m'zipata izi kuti mugwadire Yehova.

3. Yehova wa makamu atero, Mulungu wa Israyeli, Konzani njira zanu ndi macitidwe anu, ndipo ndidzakukhalitsani inu m'malo ano.

4. Musakhulupirire mau onama, kuti, Kacisi wa Yehova, kacisi wa Yehova, kacisi wa Yehova ndi awa.

5. Pakuti mukakonzatu njira zanu ndi macitidwe anu; ndi kuweruzatu milandu ya munthu ndi mnansi wace;

6. ndi kuleka kutsendereza mlendo, ndi wamasiye, ndi mkazi wamasiye, osakhetsa mwazi wosacimwa m'malo muno, osatsata milungu yina ndi kudziipitsa nayo;

7. ndipo ndidzakukhazikani inu m'malo muno, m'dziko limene ndinapatsa makolo anu, kuyambira kale lomwe kufikira muyaya,

8. Taonani, mukhulupirira mau onama, osapindulitsa.

9. Kodi mudzapha, ndi kuba, ndi kucita cigololo, ndi kulumbira zonama, ndi kupereka nsembe kwa Baala, ndi kutsata milungu yina imene simunaidziwa,

10. ndi kudza ndi kuima pamaso panga m'nyumba yino, imene ichedwa dzina langa, ndi kuti, Talanditsidwa; kuti mucite zonyansa izi?

11. Kodi nyumba yino, imene ichedwa dzina langa, ikhala phanga la okwatula pamaso panu? Taona, Ine ndaciona, ati Yehova.

12. Koma pitani tsopano ku malo anga amene anali m'Silo, m'mene ndinaikamo dzina langa poyamba paja, ndi kuona cimene ndinacitira cifukwa ca zoipa za anthu anga Israyeli.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 7