Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 6:6-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Pakuti Yehova wa makamu atero, Dulani mitengo, unjikani nthumbira pomenyana ndi Yerusalemu; mudzi wakudzalangidwa ndi uwu; m'kati mwace modzala nsautso.

7. Monga kasupe aturutsa madzi ace, camweco aturutsa zoipa zace; ciwawa ndi kufunkha zimveka m'kati mwace; pamaso panga masiku onse pali kulira ndi mabala.

8. Ulangizidwe, Yerusalemu, ungakucokere moyo wanga, ndingakuyese iwe bwinja, dziko losakhalamo anthu.

9. Yehova wa makamu atero, Adzakunkha otsalira a Israyeli monga mpesa; bweza dzanja lako monga wakuchera mphesa m'mitanga yace.

10. Ndidzanena ndi yani, ndidzacita mboni kwa yani, kuti amve? Taona khutu lao liri losadulidwa, ndipo sangathe kumva; taona, mau a Yehova awatonzetsa iwo; sakondwera nao.

11. Cifukwa cace ndadzala ndi ukali wa Yehova; ndalema ndi kudzikaniza; tsanulirani pa ana a pabwalo, ndi pa masonkhano a anyamata, pakuti ngakhale mwamuna ndi mkazi wace adzatengedwa, okalamba ndi iye amene acuruka masiku ace.

12. Nyumba zao zidzasanduka za ena, pamodzi ndi minda yao ndi akazi ao; pakuti ndidzatambasula dzanja langa pa okhala m'dziko, ati Yehova.

13. Pakuti kuyambira wamng'ono kufikira wamkuru onse akhala akusirira; ndiponso kuyambira mneneri kufikira wansembe onse acita monyenga,

14. Ndiponso apoletsa bala la anthu anga pang'onong'ono, ndi kuti, Mtendere, mtendere; koma palibe mtendere.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 6