Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 6:23-30 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

23. Agwira uta ndi nthungo; ali ankharwe, alibe cifundo; mau ao aphokosera ngati nyanja, akwera pa akavalo; aguba monga anthu ofuna kumenyana nkhondo ndi iwe, mwana wamkazi wa Ziyoni.

24. Tamva ife mbiri yace; manja athu alefuka, yatigwira nkhawa ndi zowawa ngati za mkazi wobala.

25. Usaturukire kumunda, usayenda m'njira; pakuti lupanga la amaliwongo ndi mantha ali m'mbali zonse.

26. Iwe mwana wamkazi wa anthu anga, udzibveke ndi ciguduli, ndi kubvimbvinika m'phulusa; ulire maliro ngati a mwana wamwamuna wa yekha, kulira kowawa koposa; pakuti wakufunkha adzatifikira ife motidzidzimutsa.

27. Ndakuyesa iwe nsanja ndi linga mwa anthu anga, kuti udziwe ndi kuyesa njira yao.

28. Onse ali opikisana ndithu, ayendayenda ndi maugogodi; ndiwo mkuwa ndi citsulo; onsewa acita mobvunda;

29. mbvukuto yatenthedwa ndi moto; mthobvu watha ndi moto wa ng'anjo; ayenga cabe; pakuti oipa sacotsedwa.

30. Anthu adzawacha nthale ya siliva, pakuti Yehova wakana iwo.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 6