Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 6:10-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Ndidzanena ndi yani, ndidzacita mboni kwa yani, kuti amve? Taona khutu lao liri losadulidwa, ndipo sangathe kumva; taona, mau a Yehova awatonzetsa iwo; sakondwera nao.

11. Cifukwa cace ndadzala ndi ukali wa Yehova; ndalema ndi kudzikaniza; tsanulirani pa ana a pabwalo, ndi pa masonkhano a anyamata, pakuti ngakhale mwamuna ndi mkazi wace adzatengedwa, okalamba ndi iye amene acuruka masiku ace.

12. Nyumba zao zidzasanduka za ena, pamodzi ndi minda yao ndi akazi ao; pakuti ndidzatambasula dzanja langa pa okhala m'dziko, ati Yehova.

13. Pakuti kuyambira wamng'ono kufikira wamkuru onse akhala akusirira; ndiponso kuyambira mneneri kufikira wansembe onse acita monyenga,

14. Ndiponso apoletsa bala la anthu anga pang'onong'ono, ndi kuti, Mtendere, mtendere; koma palibe mtendere.

15. Kodi anakhala ndi manyazi pamene anacita conyansa? lai, sanakhala konse ndi manyazi, sanathe kunyala; cifukwa cace adzagwa mwa iwo akugwa; panthawi pamene ndidzafika cwa iwo, aclzagwetsedwa, ati Yehova.

16. Yehova atero, Imani m'njira ndi kuona, funsani za mayendedwe akale, m'menemo muli njira yabwino, muyende m'menemo, ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu; koma anati, Sitidzayendamo.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 6