Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 52:29-34 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

29. caka cakhumi ndi cisanu ndi citatu ca Nebukadirezara iye anatenga ndende kucokera m'Yerusalemu anthu mazana asanu ndi atatu kudza makumi atatu ndi awiri;

30. caka ca makumi awiri ndi zitatu ca Nebukadirezara Nebuzaradani kapitao wa alonda anatenga ndende Ayuda mazana asanu ndi awiri kudza makumi anai ndi asanu; anthu onse anali zikwi zinai kudza mazana asanu ndi limodzi.

31. Ndipo panali caka ca makumi atatu ndi zisanu ndi ziwiri ca undende wa Yehoyakimu mfumu ya Yuda, mwezi wakhumi ndi iwiri, tsiku la makumi awiri ndi asanu la mwezi, Evili-Merodaki mfumu ya ku Babulo anaweramutsa mutu wa Yehoyakimu mfumu ya Yuda, namturutsa iye m'ndende;

32. nanena naye bwino, naika mpando wace upose mipando ya mafumu amene anali naye m'Babulo.

33. Ndipo anapindula zobvala zace za m'ndende, ndipo sanaleka kudya pamaso pace masiku onse a moyo wace.

34. Koma phoso lace mfumu ya ku Babulo sanaleka kumpatsa, phoso tsiku ndi tsiku gawo lace, mpaka tsiku la kufa kwace, masiku onse a moyo wace.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 52