Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 52:1-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Zedekiya anali wa zaka makumi awiri kudza cimodzi pamene analowa ufumu wace; ndipo analamulira m'Yerusalemu zaka khumi kudza cimodzi; dzina la amace ndi Hamutala mwana wamkazi wa Yeremiya wa ku Libina.

2. Ndipo iye anacita zoipa pamaso pa Yehova, monga mwa zonse anazicita Yehoyakimu.

3. Pakuti zonse zinacitika m'Yerusalemu ndi m'Yuda cifukwa ca mkwiyo wa Yehova, mpaka anawacotsa pamaso pace; ndipo Zedekiya anampandukira mfumu ya Babulo.

4. Ndipo panaoneka caka cacisanu ndi cinai ca ufumu wace mwezi wakhumi, tsiku lakhumi la mwezi, Nebukadirezara mfumu ya ku Babulo anafika, iye ndi nkhondo yace, kuti amenyane ndi Yerusalemu, ndipo anammangira zitando; ndipo anammangira malinga pozungulira pace.

5. Ndipo mudzi unazingidwa mpaka caka ca khumi ndi cimodzi ca mfumu Zedekiya.

6. Mwezi wacinai, tsiku lacisanu ndi cinai la mwezi, njala inabvuta m'mudzi, ndipo anthu a m'dziko analibe zakudya.

7. Pamenepo anaboola mudzi, ndipo anathawa amuna onse a nkhondo, naturuka m'mudzi usiku pa njira ya kucipata ca pakati pa makoma awiri, imene inali pa munda wa mfumu; Akasidi alikumenyana ndi mudzi pozungulira pace, ndipo anapita njira ya kucidikha.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 52