Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 51:27-33 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

27. Kwezani mbendera m'dziko, ombani lipenga mwa amitundu, konzerani amitundu amenyane naye, mummemezere maufumu a Ararati, Mini, ndi Asikenaza; muike nduna; amenyane naye; mukweretse akavalo ngati mandowa.

28. Konzerani amitundu amenyane ndi iye, mafumu a Amedi, akazembe ace, ndi ziwanga zace zonse, ndi dziko lonse la ufumu wace.

29. Dziko linthunthumira ndi kuphwetekedwa, pakuti zimene Yehova analingalirira Babulo ziripobe, zoti ayese dziko la Babulo bwinja lopanda wokhalamo.

30. Olimba a ku Babulo akana kumenyana, akhala m'malinga ao; mphamvu yao yalephera; akhala ngati akazi; nyumba zace zapsya ndi moto; akapici ace atyoka.

31. Wamtokoma mmodzi adzathamanga kukakomana ndi mnzace, ndi mthenga mmodzi kukomana ndi mnzace, kukauza mfumu ya ku Babulo kuti mudzi wace wagwidwa ponsepo;

32. pamadooko patsekedwa, pamatamanda a mabango patenthedwa ndi moto, ndi anthu a nkhondo aopa.

33. Pakuti atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli: Mwana wamkazi wa Babulo akunga dwale pamene aliunda; patsala kanthawi kakang'ono, ndipo nthawi yamasika idzamfikira iye.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 51