Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 5:23-31 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

23. Koma anthu awa ali ndi mtima woukirana ndi wopikisana; anapanduka nacoka.

24. Ndipo sanena m'mtima mwao, Tiopetu Yehova Mulungu wathu wopatsa mvula yoyamba ndi yamasika, m'nyengo yace; atisungira ife masabata olamulidwa a masika.

25. Mphulupulu zanu zacotsa zimenezi, ndi zocimwa zanu zakukanitsani inu zinthu zabwino.

26. Pakuti mwa anthu anga aoneka anthu oipa; adikira monga akucha misampha; acha khwekhwe, agwira anthu.

27. Monga cikwere codzala ndi mbalame, comweco nyumba zao zadzala ndi cinyengo; cifukwa cace akula, alemera,

28. Anenepa, anyezimira; inde apitiriza kucita zoipa; sanenera ana amasiye mlandu wao, kuti apindule; mlandu wa aumphawi saweruza.

29. Sindidzawalanga kodi cifukwa ca zimenezi? ati Yehova; kodi moyo wanga sudzabwezera cilango mtundu wotere?

30. Codabwitsa ndi coopsya caoneka m'dzikomo;

31. aneneri anenera monyenga nathandiza ansembe pakulamulira kwao; ndipo anthu anga akonda zotere; ndipo mudzacita ciani pomarizira pace?

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 5