Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 5:21-27 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

21. Tamvanitu ici, inu anthu opusa, ndi opanda nzeru; ali ndi maso koma osaona, ali ndi makutu koma osamva;

22. Kodi simundiopa Ine? ati Yehova: simudzanthunthumira pamaso pa Ine, amene ndinaika mcenga cilekaniro ca nyanja, ndi lemba lamuyaya kuti isapitirirepo? ndipo ngakhale mafunde ace acita gabvigabvi, alephera; ngakhale akokoma, sangathe kupitirirapo.

23. Koma anthu awa ali ndi mtima woukirana ndi wopikisana; anapanduka nacoka.

24. Ndipo sanena m'mtima mwao, Tiopetu Yehova Mulungu wathu wopatsa mvula yoyamba ndi yamasika, m'nyengo yace; atisungira ife masabata olamulidwa a masika.

25. Mphulupulu zanu zacotsa zimenezi, ndi zocimwa zanu zakukanitsani inu zinthu zabwino.

26. Pakuti mwa anthu anga aoneka anthu oipa; adikira monga akucha misampha; acha khwekhwe, agwira anthu.

27. Monga cikwere codzala ndi mbalame, comweco nyumba zao zadzala ndi cinyengo; cifukwa cace akula, alemera,

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 5