1. Thamangani inu kwina ndi kwina m'miseu ya Yerusalemu, taonanitu, dziwani, ndi kufunafuna m'mabwalo ace, kapena mukapeza munthu, kapena alipo wakucita zolungama, wakufuna coonadi; ndipo ndidzamkhululukira.
2. Ndipo ngakhale ati, Pali Yehova; komatu alumbira monama.
3. Yehova Inu, maso anu sali pacoonadi kodi? munawapanda iwo, koma sanaphwetekedwa mtima; munawatha iwo, koma akana kudzudzulidwa; alimbitsa nkhope zao koposa mwala; akana kubwera.
4. Ndipo ine ndinati, Ndithu amenewo ali aumphawi; ali opusa; pakuti sadziwa njira ya Yehova, kapena ciweruzo ca Mulungu wao.