Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 48:8-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Ndipo wakufunkha adzafikira pa midzi yonse, sudzapulumuka mudzi uli wonse; cigwa comwe cidzasakazidwa, ndipo cidikha cidzaonongedwa; monga wanena Yehova.

9. Patsani Moabu mapiko, kuti athawe apulumuke; midzi yace ikhale bwinja, lopanda wokhalamo.

10. Atembereredwe iye amene agwira nchito ya Yehova monyenga, atembereredwe iye amene abweza lupanga lace kumwazi.

11. Moabu wakhala m'mtendere kuyambira ubwana wace, wakhala pansenga, osatetekulidwa, sananke kundende; cifukwa cace makoleredwe ace alimobe mwa iye, pfungo lace silinasinthika.

12. Cifukwa cace, taonani, masiku adza, ati Yehova, amene ndidzatuma kwa iye otsanula, amene adzamtsanula iye; adzataya za mbiya zace, nadzaswa zipanda zao.

13. Ndipo Moabu adzacita manyazi cifukwa ca Kemosi, monga nyumba ya Israyeli inacita manyazi cifukwa ca Beteli amene anamkhulupirira,

14. Muti bwanji, Tiri amphamvu, olimba mtima ankhondo?

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 48