Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 48:19-31 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

19. Iwe wokhala m'Aroeri, ima panjira, nusuzumire umfunse iye amene athawa, ndi mkazi amene apulumuka; nuti, Cacitidwa ciani?

20. Moabu wacitidwa manyazi, pakuti watyoka; kuwa nulire, nunene m'Arinoni, kuti Moabu wapasuka.

21. Ciweruzo cafika pa dziko lacidikha; pa Holoni, ndi pa Yaza, ndi pa Mefati;

22. ndi pa Diboni, ndi pa Nebo, ndi pa Beti-Dibilataimu;

23. ndi pa Kiriataimu, ndi pa Beti-Gamuli, ndi pa Beti-Meoni;

24. ndi pa Kerioti, ndi pa Bozira, ndi pa midzi yonse ya dziko la Moabu, yakutari kapena yakufupi.

25. Nyanga ya Moabu yaduka, ndipo watyoka mkono wace, ati Yehova.

26. Umledzeretse iye; pakuti anadzikuza pokana Yehova; Moabu yemwe adzabvimvinika m'kusanza kwace, ndipo iye adzasekedwanso.

27. Kodi sunaseka Israyeli? Kodi iye anapezedwa mwa mbala? pakuti nthawi zonse unena za iye, upukusa mutu.

28. Inu okhala m'Moabu, siyani midzi, khalani m'thanthwe; nimukhale monga njiwa imene isanja cisanja cace pambali pakamwa pa dzenje.

29. Ife tamva kudzikuza kwa Moabu, wadzikuza ndithu, kunyang'wa kwace, ndi kunyada kwace, ndi kudzitama kwace, ndi kudzikuza kwa mtima wace.

30. Ine ndidziwa mkwiyo wace, ati Yehova, kuti uli cabe; zonyenga zace sizinacita kanthu.

31. Cifukwa cace ndidzakuwira Moabu; inde, ndidzapfuulira Moabu yense, adzalirira anthu a ku Kirere.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 48