Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 47:1-5 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Mau a Yehova amene anadza kwa Yeremiya mneneri onena za Afilisti, Farao asanakanthe Gaza.

2. Yehova atero: Taonani, madzi adzakwera kuturuka kumpoto, nadzakhala mtsinje wosefuka, nadzasefukira padziko ndi pa zonse ziri m'mwemo, pamudzi ndi pa onse okhalamo; ndipo amuna adzalira, ndi onse okhala m'dziko adzakuwa.

3. Pomveka migugu ya ziboda za olimba ane, pogumukira magareta ace, ndi pophokosera njinga zace, atate sadzaceukira ana ao cifukwa ca kulefuka kwa manja ao;

4. cifukwa ca tsiku lakudzafunkha Afilisti onse, kuphera Turo ndi Zidoni othangata onse akutsala; pakuti Yehova adzafunkha Afilisti, otsala a cisumbu ca Kafitori.

5. Dazi lafikira a Gaza; Asikeloni wathedwa, otsala m'cidikha cao; udzadziceka masiku angati?

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 47