Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 46:16-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

16. Anapunthwitsa ambiri, inde, anagwa wina pa mnzace, ndipo anati, Ukani, tinkenso kwa anthu athu, ku dziko la kubadwa kwathu, kucokera ku lupanga lobvutitsa.

17. Ndipo anapfuula kumeneko, Farao mfumu ya Aigupto ndiye phokoso lokha; wapititsa nthawi yopangira,

18. Pali Ine, ati Mfumu, dzina lace ndi Yehova wa makamu, ndithu monga Tabori mwa mapiri, monga Karimeli pambali pa nyanja, momwemo adzafika.

19. Mwana wamkazi iwe wokhala m'Aigupto, dzikonzere kunka kundende; pakuti Nofi adzakhala bwinja, nadzapsya, mulibenso wokhalamo.

20. Aigupto ndi ng'ombe ya msoti yosalala; cionongeko cituruka kumpoto cafika, cafika.

21. Ndiponso olipidwa ace ali pakati pace onga ngati ana a ng'ombe a m'khola; pakuti iwonso abwerera, athawa pamodzi, sanaime; pakuti tsiku la tsoka lao linawafikira, ndi nthawi ya kuweruzidwa kwao.

22. Mkokomo wace udzanga wa njoka yothawa; pakuti adzayenda ndi nkhondo, adzafika kumenyana naye ndi nkhwangwa, monga akutema mitengo.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 46