Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 44:1-5 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Mau amene anadza kwa Yeremiya onena za Ayuda onse amene anakhala m'dziko la Aigupto, okhala pa Migidoli, ndi pa Tapanesi, ndi pa Nofi, ndi m'dziko la Patirosi, akuti,

2. Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli: Mwaona coipa conse cimene ndatengera pa Yerusalemu, ndi pa midzi yonse ya Yuda; ndipo, taonani, lero lomwe iri bwinja, palibe munthu wokhalamo;

3. cifukwa ca coipa cao anacicita kuutsa naco mkwiyo wanga; pakuti anapita kukafukizira, ndi kutumikira milungu yina, Imene sanaidziwa, ngakhale iwo, ngakhale inu, ngakhale makolo anu.

4. Koma ndinatuma kwa inu atumiki anga onse aneneri, ndinauka mamawa ndi kuwatuma, ndi kuti, Musacitetu conyansa ici ndidana naco.

5. Koma sanamvera, sanachera khutu lao kuti atembenuke asiye coipa cao, osafukizira milungu yina.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 44