13. Koma mukati, Sitidzakhala m'dziko muno; osamvera mau a Yehova Mulungu wanu;
14. ndi kuti, Iai; tidzanka ku Aigupto, kumene sitidzaona nkhondo, sitidzamva kulira kwa lipenga, sitidzamva njala yokhumba mkate; pamenepo tidzakhala;
15. cifukwa cace mumve mau a Yehova, Otsala inu a Yuda, atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli, Ngati mulozetsa nkhope zanu kuti mulowe m'Aigupto, kukakhala m'menemo;
16. pamenepo padzakhala, kuti lupanga limene muopa lidzakupezani m'menemo m'dziko la Aigupto, ndi njala, imene muiopa, idzakuumirirani kumeneko ku Aigupto; pamenepo mudzafa.