Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 41:15-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. Koma Ismayeli mwana wace wa Netaniya anapulumuka Yohanani ndi anthu asanu ndi atatu, nanka kwa ana a Amoni.

16. Ndipo Yohanani mwana wace wa Kareya ndi akazembe onse a makamu amene anali naye, anatenga anthu onse otsala a ku Mizipa, amene anawabweza kwa Ismayeli mwana wace wa Netaniya atapha Gedaliya mwana wace wa Ahikamu, anthu a nkhondo, ndi akazi, ndi ana, ndi adindo, amene anawabwezanso ku Gibeoni;

17. ndipo anacoka, natsotsa m'Geruti-Kimamu, amene ali ku Betelehemu, kunka kulowa m'Aigupto,

18. cifukwa ca Akasidi; pakuti anawaopa, cifukwa Ismayeli mwana wace wa Netaniya anapha Gedaliya mwana wace wa Akikamu, amene mfumu ya ku Babulo anamuika wolamulira m'dzikomo.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 41