Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 41:14-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. Ndipo anthu onse amene Ismayeli anatenga ndende kuwacotsa m'Mizipa anatembenuka nabwera, nanka kwa Yohanani mwana wace wa Kareya,

15. Koma Ismayeli mwana wace wa Netaniya anapulumuka Yohanani ndi anthu asanu ndi atatu, nanka kwa ana a Amoni.

16. Ndipo Yohanani mwana wace wa Kareya ndi akazembe onse a makamu amene anali naye, anatenga anthu onse otsala a ku Mizipa, amene anawabweza kwa Ismayeli mwana wace wa Netaniya atapha Gedaliya mwana wace wa Ahikamu, anthu a nkhondo, ndi akazi, ndi ana, ndi adindo, amene anawabwezanso ku Gibeoni;

17. ndipo anacoka, natsotsa m'Geruti-Kimamu, amene ali ku Betelehemu, kunka kulowa m'Aigupto,

18. cifukwa ca Akasidi; pakuti anawaopa, cifukwa Ismayeli mwana wace wa Netaniya anapha Gedaliya mwana wace wa Akikamu, amene mfumu ya ku Babulo anamuika wolamulira m'dzikomo.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 41