Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 39:12-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Umtenge, numyang'anire bwino, usamsautse, koma umcitire monga iye adzanena nawe.

13. Ndipo Nebuzaradani kapitao wa alonda anatumiza, ndi Nebusazibani, mkuru wa adindo Rabi-Sarisi, ndi Nerigalisarezari mkuru wa alauli, ndi akuru onse a mfumu ya ku Babulo;

14. iwonso anatumiza, namcotsa Yeremiya m'bwalo la kaidi, nampereka iye kwa Gedaliya mwana wa Ahikamu, mwana wa Safani, kuti anke naye kwao; momwemo iye anakhala ndi anthu.

15. Ndipo mau a Yehova anadza kwa Yeremiya, potsekeredwa iye m'bwalo la kaidi, kuti,

16. Pita, ukanene kwa Ebedi-Meleki Mkusi, kuti, Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli: Taona, ndidzafikitsira mudzi uwu mau anga kuusautsa, osaucitira zabwino; ndipo adzacitidwa pamaso pako tsiku lomwelo.

17. Koma ndidzakupulumutsa tsiku lomwelo, ati Yehova: ndipo sudzaperekedwa m'manja a anthu amene uwaopa.

18. Pakuti ndidzakupulumutsatu ndipo sudzagwa ndi lupanga, koma udzakhala nao moyo wako ngati cofunkha, pakuti wandikhulupirira Ine, ati Yehova.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 39