Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 37:1-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Zedekiya mwana wa Yosiya anakhala mfumu m'malo a Koniya mwana wa Yehoyakimu, amene Nebukadirezara mfumu ya ku Babulo inamlowetsa mfumu m'dziko la Yuda.

2. Koma ngakhale iye, ngakhale atumiki ace, ngakhale anthu a padziko, sanamvere mau a Yehova, amene ananena mwa Yeremiya mneneri.

3. Ndipo Zedekiya mfumu anatuma Yehukali mwana wa Selemiya, ndi Zefaniya mwana wa Maseya wansembe, kwa Yeremiya mneneri, kukanena, Mutipemphereretu kwa Yehova Mulungu wathu.

4. Ndipo Yeremiya analikuyendayenda mwa anthu; cifukwa asanamuike iye m'nyumba yandende.

5. Ndipo nkhondo ya Farao inaturuka m'Aigupto; ndipo pamene Akasidi omangira misasa Yerusalemu anamva mbiri yao, anacoka ku Yerusalemu.

6. Ndipo mau a Yehova anadza kwa Yeremiya mneneri, kuti,

7. Atero Yehova, Mulungu wa Israyeli: Muzitero kwa mfumu ya Yuda, imene inakutumani inu kwa Ine kuti mundifunse Ine: Taonani, nkhondo ya Farao, yakuturukira kudzathandiza inu, idzabwerera ku Aigupto ku dziko lao.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 37