Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 35:1-6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Mau amene anadza kwa Yeremiya kucokera kwa Yehova masiku a Yehoyakimu mwana wa Yosiya, mfumu ya Yuda, kuti,

2. Pita ku nyumba ya Arekabu, nunene nao, nulowetse iwo m'nyumba ya Yehova, m'cipinda cina, nuwapatse iwo vinyo amwe.

3. Ndipo ndinatenga Yaasaniya mwana wa Yeremiya, mwana wa Habazinya, ndi abale ace, ndi ana amuna ace, ndi nyumba yonse ya Arekabu;

4. ndipo ndinawalowetsa m'nyumba ya Yehova, m'cipinda ca ana a Hanani mwana wa Igadaliya, munthu wa Mulungu, cokhala pambali pa cipinda ca akuru, ndico cosanjika pa cipinda ca Maseya mwana wa Salumu, mdindo wa pakhomo;

5. ndipo ndinaika pamaso pa ana amuna a nyumba ya Arekabu mbale zodzala ndi vinyo, ndi zikho, ndipo ndinati kwa iwo, Imwani vinyo.

6. Koma anati, Sitidzamwa vinyo; pakuti Yonadabu mwana wa Rekabu kholo lathu anatiuza ife, kuti, Musadzamwe vinyo, kapena inu, kapena ana anu, kumuyaya;

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 35