Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 32:11-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Ndipo ndinatenga kalata wogulira, wina wosindikizidwa, monga mwa lamulo ndi mwambo, ndi wina wobvundukuka;

12. ndipo ndinapereka kalata wogulirayo kwa Baruki mwana wa Neriya, mwana wa Maseya, pamaso pa Hanameli mwana wa mbale wa atate wanga, ndi pamaso pa mboni zimene zinalemba pa kalata wogulirayo, pamaso pa Ayuda onse okhala m'bwalo la kaidi.

13. Ndipo ndinauza Baruki pamaso pao, kuti,

14. Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli atero; Tenga akalata awa, kalata uyu wogulira, wosindikizidwa, ndi kalata uyu wobvundukuka, nuwaike m'mbiya yadothi; kuti akhale masiku ambiri.

15. Pakuti Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli atero: Nyumba ndi minda ndi minda yamphesa idzagulidwanso m'dziko muno.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 32