1. Nthawi yomweyo, ati Yehova, ndidzakhala Mulungu wa mabanja onse a Israyeli, ndipo iwo adzakhala anthu anga.
2. Atero Yehova, Anthu opulumuka m'lupanga anapeza cisomo m'cipululu; Israyeli, muja anakapuma.
3. Yehova anaonekera kwa ine kale, ndi kuti, Inde, ndakukonda iwe ndi cikondi cosatha; cifukwa cace ndakukoka iwe ndi kukukomera mtima.