Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 30:1-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Mau amene anadza kwa Yeremiya kucokera kwa Yehova, kuti,

2. Atero Yehova, Mulungu wa Israyeli, kuti, Lemba m'buku mau onse amene ndanena kwa iwe.

3. Pakuti, taona, masiku adzadza, ati Yehova, amene ndidzabwezanso undende wa anthu anga Aisrayeli ndi Ayuda, ati Yehova; ndipo ndidzawabwezera ku dziko limene ndinapatsa makolo ao. Ndipo adzakhala nalo.

4. Awa ndi mau ananena Yehova za Israyeli ndi Yuda.

5. Pakuti Yehova atero: Tamva ife mau akunthunthumira, ndi amantha, si amtendere.

6. Funsani tsopano, ndi kuona ngati mwamuna aona mwana; cifukwa canji ndiona mwamuna ndi manja ace pa cuuno cace, monga mkazi alinkubala, ndi nkhope zao zotumbuluka?

7. Kalanga ine! pakuti nlalikuru tsikulo, palibe lina lotere; ndi nthawi ya msauko wa Yakobo; koma adzapulumuka m'menemo.

8. Pakuti padzakhala tsiku lomwelo, ati Yehova wa makamu, kuti ndidzatyola gori lace pakhosi pako, ndipo ndidzadula zomangira zako; ndipo alendo sadzamuyesanso iye mtumiki wao;

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 30