Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 29:7-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. Nimufune mtendere wa mudzi umene ndinakutengerani am'nsinga, nimuwapempherere kwa Yehova; pakuti mwa mtendere wace inunso mudzakhala ndi mtendere.

8. Pakuti Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli atero: Aneneri anu ndi akuombeza anu amene akhala pakati panu, asakunyengeni inu, musamvere maloto anu amene mulotetsa.

9. Pakuti anenera kwa inu zonama m'dzina langa; sindinatuma iwo, ati Yehova.

10. Pakuti Yehova atero, kuti, Zitapita zaka makumi asanu ndi awiri pa Babulo, ndidzakuyang'anirani inu, ndipo ndidzakucitirani inu mau anga abwino, ndi kubwezera inu kumalo kuno.

11. Pakuti ndidziwa malingiriro amene ndilingiririra inu, ati Yehova, malingiriro a mtendere, si a coipa, akukupatsani inu adzukulu ndi ciyembekezero.

12. Pamenepo mudzandiitana Ine, ndipo mudzanka ndi kupemphera kwa Ine, ndipo ndidzakumverani inu.

13. Ndipo mudzandifuna Ine, ndi kundipeza, pamene mundifuna ndi mtima wanu wonse.

14. Ndipo ndidzapezedwa ndi inu, ati Yehova, ndidzabwezanso undende wanu, ndipo ndidzasonkhanitsa inu kwa mitundu yonse, ndi kumalo konse kumene ndinakupitikitsirani inu, ati Yehova; ndipo ndidzakubwezeraninso kumalo kumene ndinakutengani inu andende.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 29