3. Kapena adzamvera, nadzatembenuka, yense kusiya njira yace yoipa; kuti ndileke coipa, cimene ndinati ndiwacitire cifukwa ca kuipa kwa nchito zao.
4. Ndipo iwe uziti kwa iwo, Yehova atero: Ngati simudzandimvera Ine kuyenda m'cilamulo canga, cimene ndaciika pamaso panu,
5. kumvera mau a atumiki anga aneneri, amene ndituma kwa inu, pouka mamawa ndi kuwatuma iwo, koma simunamvera;
6. pamenepo ndidzayesa nyumba iyi ifanane ndi Silo, ndipo ndidzayesa mudzi uwu citemberero ca kwa mitundu yonse ya dziko lapansi.