Yehova atero: Ima m'bwalo la nyumba ya Yehova, ndi kunena kwa midzi yonse ya Yuda, imene imadza kudzagwadira m'nyumba ya Yehova, mau onse amene ndikuuza iwe kuti unene kwa iwo; usasiyepo mau amodzi.