Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 26:1-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Poyamba kukhala mfumu Yehoyakimu mwana wace wa Yosiya, mfumu ya Yuda, panadza mau awa ocokera kwa Yehova, kuti,

2. Yehova atero: Ima m'bwalo la nyumba ya Yehova, ndi kunena kwa midzi yonse ya Yuda, imene imadza kudzagwadira m'nyumba ya Yehova, mau onse amene ndikuuza iwe kuti unene kwa iwo; usasiyepo mau amodzi.

3. Kapena adzamvera, nadzatembenuka, yense kusiya njira yace yoipa; kuti ndileke coipa, cimene ndinati ndiwacitire cifukwa ca kuipa kwa nchito zao.

4. Ndipo iwe uziti kwa iwo, Yehova atero: Ngati simudzandimvera Ine kuyenda m'cilamulo canga, cimene ndaciika pamaso panu,

5. kumvera mau a atumiki anga aneneri, amene ndituma kwa inu, pouka mamawa ndi kuwatuma iwo, koma simunamvera;

6. pamenepo ndidzayesa nyumba iyi ifanane ndi Silo, ndipo ndidzayesa mudzi uwu citemberero ca kwa mitundu yonse ya dziko lapansi.

7. Ndipo ansembe ndi aneneri ndi anthu onse anamva Yeremiya alinkunena mau awa m'nyumba ya Yehova.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 26