Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 23:18-27 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

18. Pakuti ndani waima m'upo wa Yehova, kuti aone namve mau ace? ndani wazindikira mau anga, nawamva?

19. Taonani, cimphepo ca Yehova, kupsa mtima kwace, kwaturuka, inde cimphepo cozungulira; cidzagwa pamutu pa woipa.

20. Mkwiyo wa Yehova sudzabwerera, mpaka atacita, mpaka atatha maganizo a mtima wace; masiku otsiriza mudzacidziwa bwino.

21. Sindinatuma aneneri awa, koma anathamanga; sindinanena ndi iwo, koma ananenera.

22. Koma akadaima m'upo wanga, akadamvetsa anthu anga mau anga, akadatembenuza iwo ku njira yao yoipa, ndi ku coipa ca nchito zao.

23. Kodi ndine Mulungu wa pafupi, ati Yehova, si Mulungu wa patari?

24. Kodi munthu angathe kubisala mobisika kuti ndisamuone iye? ati Yehova. Kodi Ine sindidzala kumwamba ndi dziko lapansi? ati Yehova.

25. Ndamva conena aneneri, amene anenera zonama m'dzina langa, kuti, Ndalota, ndalota.

26. Ici cidzakhala masiku angati m'mtima mwa aneneri amene anenera zonama; ndiwo aneneri a cinyengo ca mtima wao?

27. amene aganizira kuti adzaiwalitsa anthu anga dzina langa, ndi maloto ao amene anena munthu yense kwa mnansi wace, monga makolo ao anaiwala dzina limene ndimcha nalo Baala.

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 23