Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yeremiya 22:19-28 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

19. Adzamuika monga kuika buru, adzamkoka nadzamponya kunja kwa zipata za Yerusalemu.

20. Kwera ku Lebano, nupfuule; kweza mau ako m'Basani; nupfuule m'Abarimu; pakuti mabwenzi ako onse atha,

21. Ndinanena ndi iwe m'phindu lako; koma unati, Sindidzamva. Awa ndi makhalidwe ako kuyambira ubwana wako, kuti sudamvera mau anga,

22. Mphepo idzadyetsa abusa ako onse, ndipo mabwenzi ako adzalowa m'ndende; ntheradi udzakhala ndi manyazi ndi kunyazitsidwa cifukwa ca coipa cako conse.

23. Iwe wokhala m'Lebano, womanga cisa cako m'mikungudza, udzacitidwa cisoni cacikuru nanga pamene mapweteko adzadza kwa iwe, monga mkazi alinkudwala!

24. Pali ine, ati Yehova, ngakhale Koniya mwana wace wa Yehoyakimu mfumu ya Yuda akadakhala mphete ya pa dzanja langa lamanja, ndikadacotsa iwe kumeneko;

25. ndipo ndidzakupereka iwe m'dzanja la iwo amene afuna moyo wako, m'dzanja la iwo: amene uwaopa, m'dzanja la Nebukadirezara mfumu ya ku Babulo, m'dzanja la Akasidi.

26. Ndipo ndidzakuturutsa iwe, ndi mai wako wakubala iwe, kulowa m'dziko lina, limene sunabadwiramo; m'menemo udzafa.

27. Koma kudziko kumene moyo wao ukhumba kubwerera, kumeneko sadzabwerako.

28. Kodi munthu uyu Koniya ndiye mbiya yopepuka yosweka? Kodi ndiye mbiya yosakondweretsa? cifukwa canji aturutsidwa iye, ndi mbeu zace, ndi kuponyedwa m'dziko limene salidziwa?

Werengani mutu wathunthu Yeremiya 22